Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 1:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwace, imtetezere.

5. Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.

6. Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zace.

7. Ndipo ana a Aroni asonkhe mota pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;

8. ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe;

9. koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

10. Ndipo copereka cace cikakhala ca nkhosa, kapena ca mbuzi, cikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda cirema.

11. Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

12. Ndipo aikadzule ziwalo zace, pamodzi ndi mutu wace ndi mafuta ace; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe.

13. Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

14. Ndipo copereka cace ca kwa Yehova cikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera naco copereka cace cikhale ca njiwa, kapena ca maunda.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 1