Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 9:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ace, nati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi.

2. Kuopsya kwanu, ndi kucititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

3. Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

4. Koma nyama, m'mene muli moyo wace, ndiwo mwazi wace, musadye.

5. Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wace wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.

6. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m'cifanizo ca Mulungu Iye anampanga munthu.

7. Ndi inu, mubalane, mucuruke; muswane pa dziko lapansi, nimucuruke m'menemo.

8. Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ace pamodzi naye, kuti,

9. Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;

10. ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zoturuka m'cingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi,

11. Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamarizidwanso konse ndi madzi a cigumula; ndipo sikudzakhalanso konse cigumula cakuononga dziko lapansi.

12. Ndipo anati Mulungu, Ici ndici cizindikiro ca pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, ku mibadwo mibadwo;

13. ndiika Uta-wa-Leza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala cizindikiro ca pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 9