Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 48:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awaphe dzina la abale ao m'colowa cao.

7. Tsono ine, pamene ndinacokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu).

8. Ndipo Israyeli anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa?

9. Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.

10. Koma maso a Israyeli anali akhungu m'ukalamba wace, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

11. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.

12. Ndipo Yosefe anaturutsa iwo pakati pa maondo ace, nawerama ndi nkhope yace pansi.

13. Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efraimu m'dzanja lace lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lace lamanzere ku dzanja lamanja la Israyeli, nadza nao pafupi ndi iye.

14. Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.

15. Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pace anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isake, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,

16. mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa lichulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isake; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi.

17. Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wace anaika dzanja lace lamanja pa mutu wa Efraimu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wace, kulicotsa pa mutu wa Efraimu ndi kuliika pa muta wa Manase.

18. Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Msatero atate wanga, cifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 48