Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 47:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Citatha caka cimeneco, anadza kwa iye caka caciwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe oza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;

19. tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? mutigule ife ndi dziko lathu ndi cakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.

20. Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Aigupto, cifukwa Aaigupto anagulitsa yense munda wace, cifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.

21. Tsono anthu, anasunthira iwo ku midzi kucokera kumphepete kwa malire a Aigupto kufikira kumphepete kwina kwace.

22. Koma dziko la ansembe lokha sanagule, cifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; cifukwa cace sanagulitsa dziko lao.

23. Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu sizi, mubzale m'dziko.

24. Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za cakudya canu, ndi ca ana anu ndi mabanja anu.

25. Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.

26. Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Aigupto kuukira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao.

27. Ndipo Israyeli anakhala m'dziko la Aigupto, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nacuruka kwambiri.

28. Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Aigupto zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wace zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.

29. Ndipo nthawi inayandikira kuti Israyeli adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wace wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga, nundicitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Aigupto;

Werengani mutu wathunthu Genesis 47