Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 38:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma cimene iye anacita cinali coipa pamaso pa Mulungu, ndipo anamupha iyenso.

11. Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpengozi wace, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna; cifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ace. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wace.

12. Atacuruka masiku mwana wamkazi wa Sua, mkazi wace wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zace ku Timna, iye ndi bwenzi lace Hira, M-adulami.

13. Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zace.

14. Pamenepo anabvula zobvala zacezamasiye, nadzipfundandi copfunda cace, nabvala nakhala pa cipata ca Enaimu, cifukwa ciri pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatsa iye kuti akhale mkazi wace.

15. Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: cifukwa iye anabisa nkhope yace.

16. Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; cifukwa sanamdziwa kuti ndiye mpongozi wace. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine ciani kuti ulowane ndi ine.

17. Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine cikole mpaka ukatumiza?

18. Ndipo iye anati, Cikole canji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi cingwe cako, ndi ndodo iri m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 38