Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:29-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe comwe ndakutumikira iwe ndi comwe zacita zoweta zako ndi ine.

30. Cifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zacuruka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kuli konse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

31. Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandicitira ine cotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.

32. Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse ndi kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathotho-mathotho ndi zamaanga-maanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamaangamaanga ndi zamathotho-mathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33. Cotero cilungamo canga cidzandibvomereza m'tsogolomo, pamene udzandifika cifukwa ca malipiro amene ali patsogolo pako; iri yonse yosakhala yamathotho-mathotho ndi yamaanga-maanga ya mbuzi, ndi iri yonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34. Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35. Tsiku lomwelo Labani anacotsa atonde amene anali amipyololo-mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ace amuna.

36. Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

37. Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

38. Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'micera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo, ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

39. Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathotho-mathotho, ndi zamaanga-maanga.

40. Ndipo Yakobo analekanitsa ana a nkhosa naziika nkhope za zoweta kuti ziyang'anire zamipyololo-mipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani, ndipo anaika magulu ace pa okha; sanaziika pa zoweta za Labani.

41. Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'miceramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30