Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 27:34-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Pamene Esau anamva mau a atate wace Isake, analira ndi kulira kwakukuru ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wace, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.

35. Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.

36. Ndipo iye anati, Kodi si ndico cifukwa anamucha dzina lace Yakobo? kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi smunandisungira ine mdalitso?

37. Ndipo anayankha Isake nati kwa Esau, paona, ndamuyesa iye mkuru wako, ndi abale ace onse ndampatsa iye akhale akapolo ace; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakucitira iwe ciani?

38. Ndipo Esau anati kwa atate wace, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga, Ndipo Esau anakweza mau ace nalira.

39. Ndipo Isake atate wace anayankha nati kwa iye,Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi,Mpa mame a kumwamba akudzera komwe;

40. Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wamphwako;Ndipo padzakhalapamene udzapulumuka,Udzacotsa gori lace pakhosi pako.

41. Ndipo Esau anamuda Yakobo cifukwa ca mdalitso umene atate wace anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwace, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.

42. Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wace wamkuru: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wace wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkuru wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wace kuti adzakupha iwe.

43. Ndipo tsopane mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harana;

44. ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka wamcokera ukali wa mkuru wako;

45. mpaka wakucokera mkwiyo wa mkuru wako, kuti aiwale cimene wamcitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?

46. Ndipo anati Rebeka kwa Isake, Ndalema moyo wanga cifukwa ca aria akazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana akazi a Heti, onga ana akazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?

Werengani mutu wathunthu Genesis 27