Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:43-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene aturuka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;

44. ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamila zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.

45. Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anaturuka ndi mtsuko wace pa phewa lace, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.

46. Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lace, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamila.

47. Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pace ndi zingwinjiri pa manja ace.

48. Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wace mwana wamkazi wa mphwace wa mbuyanga.

49. Tsopano, ngati mudzamcitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.

50. Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Caturuka kwa Yehova cinthu ici; sitingathe kunena ndi iwe coipa kapena cabwino.

51. Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.

52. Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi,

53. Ndipo mnyamatayo anaturutsa zokometsera zasiliva ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatari kwa mlongo wace ndi amace.

54. Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

55. Ndipo mlongo wace ndi amace anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pace iye adzamuka.

56. Ndipo iye anati kwa iwo, Musandicedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

57. Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24