Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m'zinthu zonse.

2. Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wace wamkuru wa pa nyumba yace, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga:

3. ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana akazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.

4. Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi.

5. Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwacokera inu?

6. Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.

7. Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

8. Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.

9. Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lace pansi pa ncafu yace ya Abrahamu mbuye wace, namlumbirira iye za cinthuco.

10. Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyace, namuka: cifukwa kuti cuma conse ca mbuyace cinali m'dzanja lace: ndipo anacoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori.

11. Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.

12. Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumcitire ufulu mbuyanga Abrahamu,

13. Taonani, ine ndiima pa citsime ca madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi aturuka kudzatunga madzi;

14. ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.

15. Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24