Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 22:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.

9. Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isake mwana wace, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.

10. Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lace, natenga mpeni kuti amuphe mwana wace.

11. Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.

12. Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamcitire iye kanthu; cifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.

13. Ndipo Abrahamu anatukula maso ace nayang'ana taonani, pambuyo pace nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zace m'ciyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wace.

14. Ndipo Abrahamu anacha dzina lace la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova cidzaoneka.

15. Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kaciwiri,

16. nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wadta ici, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wa yekha,

17. kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kucurukitsa ndidzacurukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mcenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa cipata ca adani ao;

18. m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lap ansi idzadalitsidwa: cifukwa wamvera mau anga.

19. Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ace, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.

20. Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;

21. Huzi woyamba ndi Buzi mphwace, ndi Kemueli atate wace wa Aramu;

Werengani mutu wathunthu Genesis 22