Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:16-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

17. Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi,

18. nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabino.

19. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacinai.

20. Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zocuruka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga.

21. Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikuru ndi zoyendayenda zamoyo zakucuruka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wace: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

22. Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zicuruke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zicuruke pa dziko lapansi.

23. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu.

24. Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

25. Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wace, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

26. Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

27. Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

28. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 1