Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 45:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. M'dzikomo ili lidzakhala lace lace m'Israyeli; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israyeli monga mwa mapfuko ao.

9. Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kucita ciwawa, ndi kulanda za eni ace; mucite ciweruzo ndi cilungamo; lekani kupitikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.

10. Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona.

11. Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.

12. Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo mane wanu.

13. Copereka mucipereke ndico limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele;

14. ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri;

15. ndi mwana wa nkhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wocokera ku madimba a Israyeli, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwacitira cotetezera, ati Ambuye Yehova.

16. Anthu onse a m'dziko azipereka copereka ici cikhale ca kalonga wa m'Israyeli.

17. Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pamadyerero, ndi pokhala mwezi, ndi pamasabata; pa madyerero onse oikika a nyumba ya Israyeli; ndipo apereke nsembe yaucimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kucitira cotetezera nyumba ya Israyeli.

18. Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndipo uyeretse malo opatulika.

19. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo, naupake pa mphuthu za kacisi, ndi pa ngondya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za cipata ca bwalo lam'kati.

20. Tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo ucitire momwemo ali yense wolakwa ndi wopusa; motero mucitire kacisiyo comtetezera.

21. Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, muzicita Paskha, madyerero a masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda cotupitsa.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 45