Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo, naupake pa mphuthu za kacisi, ndi pa ngondya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za cipata ca bwalo lam'kati.