Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 37:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobede gobede, ndi mafupa anasendererana, pfupa kutsata pfupa linzace.

8. Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pace; koma munalibe mpweya mwa iwo.

9. Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kucokera ku mphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.

10. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira ciriri, gulu la nkhondo lalikurukuru ndithu.

11. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israyeli; taonani, akuti, Mafupa athu auma, ciyembekezo cathu catayika, talikhidwa.

12. Cifukwa cace, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu muturuke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 37