Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 37:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anaturuka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa cigwa, ndico codzala ndi mafupa;

2. ndipo anandipititsa pamenepo pozungulira ponse, ndipo taonani, anali aunyinji pacigwa pansi, ndipo anaumitsitsa.

3. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.

4. Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova.

5. Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo.

6. Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehoya.

7. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobede gobede, ndi mafupa anasendererana, pfupa kutsata pfupa linzace.

8. Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pace; koma munalibe mpweya mwa iwo.

9. Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kucokera ku mphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.

10. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira ciriri, gulu la nkhondo lalikurukuru ndithu.

11. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israyeli; taonani, akuti, Mafupa athu auma, ciyembekezo cathu catayika, talikhidwa.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 37