Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 20:34-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo ndidzakuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.

35. Ndipo ndidzalowa nanu m'cipululu ca mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.

36. Monga ndinaweruza makolo anu m'cipululu ca dziko la Aigupto, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.

37. Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'cimango ca cipangano;

38. ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawaturutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israyeli; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39. Ndipo inu, nyumba ya Israyeli, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ace, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.

40. Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothubvuka la Israyeli, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israyeli, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.

41. Ngati pfungo lokoma ndidzakulandirani pakukuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukucotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

42. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dzil ko la Israyeli, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.

43. Ndi pomwepo mudzakumbukila njira zanu, ndi zonse mudazicita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, cifukwa ca zoipa zanu zonse mudazicita.

44. M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditacita nanu cifukwa ca dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa macitidwe anu obvunda, nyumba ya Israyeli inu, ati Ambuye Yehova.

45. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

46. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango ya kuthengo la kumwera kwa Yuda;

47. nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uli wonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uli wonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.

48. Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika.

49. Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! anandinena, Wonena mafanizo uyu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 20