Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 20:27-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Cifukwa cace wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa icinso atate anu anandicitira mwano pakundilakwira Ine.

28. Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya citunda ciri conse cacitali, ndi mtengo uli wonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, napetekapo nsembe zao zondiputa, aponso anacita pfungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.

29. Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lace lichedwa Msanje, mpaka lero lino.

30. Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anacitira makolo anu? mucita cigololo kodi kutsata zonyansa zao?

31. ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israyeli? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;

32. ndi ici cimauka mumtima mwanu sicidzacitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.

33. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.

34. Ndipo ndidzakuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.

35. Ndipo ndidzalowa nanu m'cipululu ca mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.

36. Monga ndinaweruza makolo anu m'cipululu ca dziko la Aigupto, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.

37. Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'cimango ca cipangano;

38. ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawaturutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israyeli; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39. Ndipo inu, nyumba ya Israyeli, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ace, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.

40. Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothubvuka la Israyeli, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israyeli, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.

41. Ngati pfungo lokoma ndidzakulandirani pakukuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukucotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

42. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dzil ko la Israyeli, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 20