Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 4:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukacite nayo zizindikilozo.

18. Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wace, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kumka kwa abale anga amene ali m'Aigupto, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

19. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'Midyani, Muka, bwerera kumka ku Aigupto; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.

20. Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.

21. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire ucite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wace kuti asadzalole anthu kupita.

22. Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova, Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israyeli.

23. Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.

24. Ndipo kunali panjira, kucigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.

25. Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo iye anamleka.

26. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, cifukwa ca mdulidwe.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 4