Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Nsaru zocingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.

17. Ndipo makamwa a nsici anali amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda Iyace zasiliva; ndi zokutira mitu yace zasiliva; ndi nsici zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.

18. Ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo ndiyo nchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mu kupingasa kwace mikono isanu, yolingana ndi nsaru zocingira za pabwalo.

19. Ndi nsici zace zinali zinai, ndi makamwa ace anai, amkuwa; zokowera zace zasiliva, ndi zokutira mitu yace ndi mitanda yace zasiliva.

20. Ndi ziciri zonse za cihema, ndi za bwalo lace pozungulira, nza mkuwa.

21. Ici ndi ciwerengo ca zinthu za cihema, cihema ca mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, acite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.

22. Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose.

23. Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

24. Golidi yense anacita naye mu nchito yonse ya malo opatulika, golidi wa coperekaco, ndico matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

25. Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli cikwi cimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika;

26. munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kumka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38