Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 3:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Molungu wa makolo anu, Molungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Molungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili nw dzina langa nthawi yosatha, ici ndi cikumbukiro canga m'mibadwo mibadwo.

16. Muka, nukasonkhanitse akuru a Israyeli, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, ndi kuti; Ndakuzondani ndithu, ndi kuona comwe akucitirani m'Aigupto;

17. ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukuturutsani m'mazunzo a Aigupto, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

18. Ndipo adzamveca mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akuru a Israyeli, kwa mfumu ya Aigupto, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.

19. Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aigupto siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.

20. Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aigupto ndi zozizwa zanga zonse ndizicita pakati pace; ndi pambuyo pace adzakulolani kumuka.

21. Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Aigupto; ndipo kudzakhala, pamene muturuka simudzaturuka opanda kanthu;

22. koma mkazi yense adzafunse mnzace, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwace, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala; ndipo mudzabveke nazo ana anu amuna ndi akazi; ndipo mudzafunkhe za Aaigupto.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 3