Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 18:14-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo pamene mpongozi wace wa Mose anaona zonsezi iye anawacitira anthu, anati, Cinthu ici nciani uwacitira anthuci? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala ciriri pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?

15. Ndipo Moce anati kwa mpongozi wace, Cifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;

16. akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wace, ndi kuti ndiwadziwitsemalemba a Mulungu, ndi malamulo ace.

17. Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Cinthu ucitaci siciri cabwino ai.

18. Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti cikulaka cinthu ici; sungathe kucicita pa wekha.

19. Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo mirandu kwa Mulungu;

20. nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi nchito imene ayenera kucita.

21. Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la cinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akuru a pa zikwi, akuru a pa mazana, akuru a pa makumi asanu, akuru a pa makumi;

22. ndipo iwo aweruze mirandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti mirandu yaikuru yonse abwere nayo kwa iwe; koma mirandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakucepera nchito, ndi iwo adzasenza nawe.

23. Ukacite cinthuci, ndi Mulungu akakuuza cotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.

24. Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wace, nacita zonse adazinena.

25. Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisrayeli onse, nawaika akuru a pa anthu, akuru a pa zikwi, akuru a pa mazana, akuru a pa makumi asanu, ndi akuru a pa makumi.

26. Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwalaka amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.

27. Ndipo Mose analola mpongozi wace amuke; ndipo anacoka kumka ku dziko lace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 18