Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 15:13-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mwa cifundo canu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;Mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera.

14. Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;Kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya.

15. Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa;Agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Moabu;Okhala m'Kanani onse asungunukamtima.

16. Kuopa kwakukuru ndi mantha ziwagwera;Pa dzanja lanu lalikuru akhala cete ngati mwala;Kufikira apita anthu anu, Yehova,Kufikira apita anthu amene mudawaombola.

17. Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la colowa canu,Pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova,Malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.

18. Yehova adzacita ufumu nthawi yomka muyaya.

19. Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magareta ace ndi apakavalo ace, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja.

20. Ndipo Miriamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lace; ndipo akazi onse anaturuka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.

21. Ndipo Miriamu anawayankha,Yimbirani Yehova, pakuti wapambanatu;Kavalo ndi wokwera wace anawaponya m'nyanja.Madzi a ku Mara.

22. Ndipo Mose anatsogolera Israyeli kucokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anaturukako nalowa m'cipululu ca Suri; nayenda m'cipululu masiku atatu, osapeza madzi.

23. Pamene anafika ku Mara, sanakhoza kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; cifukwa cace anacha dzina lace Mara.

24. Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa ciani?

25. Ndipo iye anapfuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi ciweruzo, ndi pomwepa anawayesa;

26. ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kucita zoona pamaso pace, ndi kuchera khutu pa malamulo ace, ndi kusunga malemba ace onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aaigupto sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuciritsa iwe.

27. Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga cigono cao pomwepo pa madziwo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 15