Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:57-68 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

57. ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.

58. Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;

59. Yehova adzacita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwiza, miliri yaikuru ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.

60. Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.

61. Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la cilamulo ici, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.

62. Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mukacuruka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

63. Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukucitirani zabwino, ndi kukucurukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.

64. Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.

65. Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.

66. Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzacita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.

67. M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! ndi madzulo mudzati, Mwenzi utafika m'mawa! cifukwa ca mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi cifukwa ca zopenya maso anu zimene mudzazipenya.

68. Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogulainu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28