Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:52-65 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

53. Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.

54. Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu diso lace lidzaipira mbale wace, ndi mkazi wa pa mtima wace, ndi ana ace otsalira;

55. osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ace alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse.

56. Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;

57. ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.

58. Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;

59. Yehova adzacita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwiza, miliri yaikuru ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.

60. Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.

61. Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la cilamulo ici, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.

62. Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mukacuruka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

63. Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukucitirani zabwino, ndi kukucurukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.

64. Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.

65. Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28