Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 12:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lace akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.

22. Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko cimodzimodzi.

23. Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yace.

24. Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.

25. Musamadya uwu; kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakucita inu zoyenera pamaso pa Yehova.

26. Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasanka;

27. ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yace muidye.

28. Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pocita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29. Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 12