Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 12:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwacita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanu lanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi.

2. Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri atali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;

3. nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao licoke m'malomo.

4. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.

5. Koma ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mapfuko anu onse kuikapo dzina lace, ndiko ku cokhalamo cace, muzifunako, ndi kufikako;

6. ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;

7. ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.

8. Musamadzacita monga mwa zonse tizicita kuno lero, yense kucita ciri conse ciyenera m'maso mwace;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 12