Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 7:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pambuyo pace ndinapenya ndi kuona cina ngati nyalugwe, cinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pace, ciromboco cinali nayonso mitu inai, nicinapatsidwa ulamuliro.

7. Pambuyo pace ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona cirombo cacinai, coopsa ndi cocititsa mantha, ndi camphamvu coposa, cinali nao mano akuru acitsulo, cinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza cotsala ndi mapazi ace; cinasiyana ndi zirombo zonse zidacitsogolera; ndipo cinali ndi nyanga khumi.

8. Ndinali kulingirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga yina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pace zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikuru.

9. Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yacifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zobvala zace zinali za mbu ngati cipale cofewa, ndi tsitsi la pa mutu pace ngati ubweya woyera, mpando wacifumu unali malawi amoto, ndi njinga zace moto woyaka.

10. Mtsinje wamoto unayenda woturuka pamaso pace, zikwi zikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pace, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.

11. Pamenepo ndinapenyera cifukwa ca phokoso la mau akuru idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adacipha ciromboci, ndi kuononga mtembo wace, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.

12. Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.

13. Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.

14. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.

15. Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.

16. Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:

17. Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.

18. Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.

Werengani mutu wathunthu Danieli 7