Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 11:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ine, caka coyamba ca Dariyo Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.

2. Ndipo tsopano ndikufotokozera coonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Perisiya, ndi yacinai idzakhala yoletnera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwace idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Helene.

3. Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzacita ufumu ndi ulamuliro waukuru, nidzacita monga mwa cifuniro cace.

4. Ndipo pakuuka iye ufumu wace udzatyoledwa, nudzagawikira ku mphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yace akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wace anacita ufumu nao; pakuti ufumu wace udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.

5. Ndipo mfumu ya kumwela, ndiye wina wa akalonga ace, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wace ndi ulamuliro waukuru.

6. Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwela adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lace; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lace; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.

7. Koma apo pophukira mizu yace adzauka wina m'malo mwace, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzacita molimbana nao, nadzawalaka;

8. ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zace zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

9. Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwela, koma adzabwera m'dziko lace lace.

10. Ndi ana ace adzacita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akuru ocuruka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzacita nkhondo mpaka linga lace.

11. Ndi mfumu ya kumwela adzawawidwa mtima, nadzaturuka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukuru; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lace.

12. Ndipo ataucotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wace; ndipo adzagwetsa zikwi makumi makumi, koma sadzalakika.

Werengani mutu wathunthu Danieli 11