Ndi ana ace adzacita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akuru ocuruka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzacita nkhondo mpaka linga lace.