Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yoabu anabwera kucokera ku nkhondo yobvumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abineri sanali ku Hebroni kwa Davide, cifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.

23. Tsono pofika Yoabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yoabu nati, Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendereo

24. Pomwepo Yoabu anadza kwa mfumu, nati, Mwacitanji? Taonani, Abineri anadza kwa inu, cifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti acokedi.

25. Mumdziwa Abineri mwana wa Neri kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kuturuka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikucita inu.

26. Ndipo Yoabu anaturuka kwa Davide, natumizira Abineri mithenga, amene anambweza ku citsime ca Sira. Koma Davide sanacidziwa.

27. Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.

28. Ndipo pambuyo pace, pakucimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osacimwira mwazi wa Abineri mwana wa Neri, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;

29. cilango cigwere pa mutu wa Yoabu ndi pa nyumba yonse ya atate wace; ndipo kusasoweke ku nyumba ya Yoabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa cakudya.

30. Motero Yoabu ndi Abisai mbale wace adapha Abineri, popeza iye adapha mbale wao Asaheli ku Gibeoni, kunkhondo.

31. Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zobvala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'cuuno, nimulire Abineri. Ndipo mfumu Davide anatsata cithatha.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3