Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Abineri anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisrayeli onse atsate inu.

13. Nati iye, Cabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira cinthu cimodzi, ndico kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Sauli, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.

14. Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Sauli, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.

15. Pomwepo Isiboseti anatumiza namcotsera kwa mwamuna wace, kwa Palitieli mwana wa Laisi.

16. Ndipo mwamuna waceyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Baburimu. Pomwepo Abineri ananena naye, Coka, bwerera; ndipo anabwerera.

17. Ndipo Abineri analankhula nao akuru a Israyeli nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;

18. citani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, a Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisrayeli ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.

19. Ndipo Abineri analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abineri anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisrayeli ndi a nyumba yonse ya Benjamini.

20. Abineri nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abineri ndi anthu okhala naye madyerero.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3