Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 2:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.

2. Comweco Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ace awiri, ndiwo Ahingamu Mjezreeli, ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.

3. Ndipo Davide anakwera nao anyamata ace okhala naye, munthu yense ndi banja lace; iwowa nakhala m'midzi ya Hebroni.

4. Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda.Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Jabezi Gileadi ndiwo amene anamuika Sauli.

5. Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Jabezi Gileadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munacitira cokoma ici mbuye wanu Sauli, ndi kumuika.

6. Ndipo tsopano Yehova acitire inu cokoma ndi coonadi; inenso ndidzakubwezerani cokoma ici, popeza munacita cinthuci.

7. Cifukwa cace tsono manja anu alimbike, nimucite camuna; pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 2