Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukile cimene mnyamata wanu ndinacita mwamphulupulu tsiku lila mbuye wanga mfumu anaturuka ku Yerusalemu, ngakhale kucisunga mumtima mfumu.

20. Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.

21. Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simeyi cifukwa ca kutemberera wodzozedwa wa Yehova?

22. Koma Davide anati, Ndiri ndi ciani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israyeli lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israyeli lero?

23. Ndipo mfumu inanena ndi Simeyi, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.

24. Ndipo Mefiboseti mwana wa Sauli anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ace, kapena kumeta ndebvu zace, kapena kutsuka zobvalazace kuyambira tsiku lomuka mfumukufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.

25. Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Cifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?

26. Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.

27. Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; cifukwa cace citani cimene cikukomerani.

28. Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjeze kudandaulira kwa mfumu?

29. Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

30. Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere ku nyumba yace.

31. Ndipo Barizilai, Mgileadi anatsika kucokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordano ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordano.

32. Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.

33. Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19