Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 17:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofeli analankhula mau akuti; ticite kodi monga mwa kunena kwace? ngati iai, unene ndiwe.

7. Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofeli suli wabwino.

8. Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ace kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga cimbalangondo cocilanda ana ace kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.

9. Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, ali yense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.

10. Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wace ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisrayeli onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.

11. Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisrayeli onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mcenga uli panyanja kucuruka kwao; ndi kuti muturuke kunkhondo mwini wace.

12. Comweco tidambvumbulukira pa malo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye.

13. Ndiponso ngati walowa ku mudzi wina, Aisrayeli onse adzabwera ndi zingwe kumudziko, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko.

14. Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israyeli anati, Uphungu wa Husai M-ariki uposa uphungu wa Ahitofeli. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofeli kuti Yehova akamtengere Abisalomucoipa.

15. Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abyatara ansembewo, Ahitofeli anapangira Abisalomu ndi akuru a Israyeli zakuti zakuti; koma ine ndinapangira zakuti zakuti.

16. Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.

17. Ndipo Jonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogeli; mdzakazi adafopita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi.

18. Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anacoka msanga onse awiri, nafika ku nyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali naco citsime pabwalo pace; ndipo anatsikira m'menemo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 17