Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ace kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga cimbalangondo cocilanda ana ace kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.