Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 16:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israyeli idzandibwezera ufumu wa atate wanga.

4. Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse ziri zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.

5. Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panaturuka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Sauli, dzina lace ndiye Simeyi, mwana wa Gera; iyeyu anaturukako, nayenda natukwana.

6. Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali kudzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwace.

7. Ndipo anatero Simeyi pakutukwana, Coka, coka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;

8. Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Sauli, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwace; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, cifukwa uli munthu wa mwazi.

9. Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Garu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wace.

10. Mfumu niti, Ndiri ndi ciani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero cifukwa ninji?

11. Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ace onse, Onani, mwana wanga woturuka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.

12. Kapena Yehova adzayang'anira cosayeneraci alikundicitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera cabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.

13. Comweco Davide ndi anthu ace anapita m'ngra, ndipo Simeyi analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza pfumbi,

14. Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko.

15. Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse amuna a Israyeli, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofeli pamodzi naye.

16. Ndipo kunali pakudza kwa Abisalomu Husai M-ariki, bwenzi la Davide, Husai ananena ndi Abisalomu, Mfumu ikhale ndi moyo, Mfumu ikhale ndi moyo.

17. Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi cimeneci ndi cifundo cako ca pa bwenzi lako? unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 16