Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo anyamata ace onse anapita naye limodzi; ndi Akereri ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kucokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.

19. Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.

20. Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? ubwerere nubwereretsenso abale ako; cifundo ndi zoonadi zikhale nawe.

21. Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.

22. Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ace onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye.

23. Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kucipululu.

24. Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la cipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kuturuka m'mudzimo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15