Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 14:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yoabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yoabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.

20. Mnyamata wanu Yoabu anacita cinthu ici kuti asandulize mamvekedwe a mranduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse ziri m'dziko lapansi.

21. Ndipo mfumuyo inanena ndi Yoabu, Taonatu, ndacita cinthu ici; cifukwa cace, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.

22. Ndipo Yoabu anagwa nkhope yace pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yoabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yacita copempha mnyamata wace.

23. Comweco Yoabu ananyamuka namka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu ku Yerusalemu.

24. Ndipo mfumu inati, Apambukire ku nyumba yaiye yekha, koma asaone nkhope yanga. Comweco Abisalomu anapambukira ku nyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.

25. Ndipo m'lsrayeli monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri cifukwa ca kukongola kwace monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wace mwa iye munalibe cirema.

26. Ndipo pometa tsitsi lace amameta potsiriza caka, cifukwa tsitsi linamlemerera, cifukwa cace atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wace, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.

27. Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lace ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.

28. Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.

29. Pamenepo Abisalomu anaitana Yoabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yaciwiri, koma anakana kubwera.

30. Cifukwa cace iye anati kwa anyamata ace, Onani munda wa Yoabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.

31. Pamenepo Yoabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu ku nyumba yace, nanena naye, Cifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;

32. Abisalomu nayankha Yoabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kucokera ku Gesuri? mwenzi nditakhala komweko; cifukwa cace tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.

33. Comweco Yoabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yace pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 14