Pamenepo Abisalomu anaitana Yoabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yaciwiri, koma anakana kubwera.