Ndipo Yoabu anagwa nkhope yace pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yoabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yacita copempha mnyamata wace.