Cifukwa cace iye anati kwa anyamata ace, Onani munda wa Yoabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.