Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 12:17-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.

18. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?

19. Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

20. Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.

21. Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,

22. Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandicitira cifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.

23. Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.

24. Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wace, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Solomo. Ndipo Yehova anamkonda iye,

25. natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namucha dzina lace Wokondedwa ndi Yehova, cifukwa ca Yehova.

26. Ndipo Yoabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wacifumu.

27. Yoabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi.

28. Cifukwa cace tsono musonkhanitseanthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungachedwe ndi dzina langa.

29. Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda.

30. Nacotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwace kunali talente wa golidi; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye naturutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri.

31. Naturutsa anthu a m'mudzimo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi nkhwangwa zacitsulo; nawapsitiriza ndi citsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kumka ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 12