Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 9:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wace; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Seba anapatsa mfumu Solomo.

10. Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomo otenga golidi ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.

11. Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oyimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.

12. Ndipo mfumu Solomo anampatsa mfumu yaikazi ya ku Seba cifuniro cace conse, ciri conse anacipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lace, iyeyu ndi anyamata ace.

13. Kulemera kwace tsono kwa golidi anafika kwa Solomo caka cimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi;

14. osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golidi ndi siliva kwa Solomo.

15. Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri za golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera golidi wonsansantha masekeli mazana awiri.

16. Napanganso malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera masekeli mazana atatu a golidi; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.

17. Mfumu inapanganso mpando wacifumu waukuru wa minyanga, naukuta ndi golidi woona.

18. Ndi mpando wacifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi copondapo mapazi cagolidi, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.

19. Ndi mikango khumi ndi iwiri Inaimirirapo, mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwa wotere m'ufumu uli wonse.

20. Ndipo zikho zomwera zonse za Solomo zinali zagolidi, ndi zipangizo zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali za golidi woona; siliva sanayesedwa kanthu m'masiku a Solomo.

21. Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golidi, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawanga mawanga.

22. Mamwemo mfumu Solomo inaposa mafumu onse a pa dziko lapansi, kunena za cuma ndi nzeru.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 9