Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 6:4-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, wakunena m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa: ndi manja ace, ndi kuti,

5. Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse m'mafuko onse a Israyeli, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu ali yense akhale kalonga wa anthu anga Israyeli;

6. koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israyeli.

7. Ndipo Davide atate wanga anafuna mumtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

8. Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti unatero mumtima mwako;

9. koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzaturuka m'cuuno mwako, Iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi.

10. Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumbayi.

11. Ndipo ndalongamo likasa, muli cipangano ca Yehova, anacicita ndi ana a Israyeli.

12. Ndipo Solomo anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israyeli, natambasula manja ace.

13. Ndipo Solomo adapanga ciunda camkuwa, m'litali mwace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, ndi msinkhu wace mikono itatu, naciika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo, nagwada pa maondo ace pamaso pa khamu lonse la Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba;

14. nati, Yehova. Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;

15. inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga cija mudamlonjezaci: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwacita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino.

16. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'cilamulo canga, monga umo unayendera iwe pamaso panga.

17. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, acitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.

18. Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?

19. Cinkana citero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kupfuula ndi kupempha kwace, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu;

20. kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.

21. Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israyeli, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululikire.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 6