Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 31:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'cilamulo ca Yehova.

5. Ndipo pobuka mau aja, ana a Israyeli anapereka mocuruka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uci, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mocuruka.

6. Ndi ana a Israyeli ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyuru miyuru,

7. Mwezi wacitatu anayamba kuika miyalo ya miyuruyi, naitsiriza mwezi wacisanu ndi ciwiri.

8. Ndipo pamene Hezekiya ndi akuru ace anadza, naona miyuruyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ace Aisrayeli.

9. Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuruyi,

10. Ndipo Azariya wansembe wamkuru wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Ciyambire anthu anabwera nazo zopereka ku nyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zatitsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ace; ndipo suku kucuruka kwa cotsala.

11. Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza.

12. Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkuru woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wace ndiye wotsatana naye.

13. Ndi Yeiyeli, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asaheli, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyeli, ndi Ismakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wace, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkuru wa ku nyumba ya Mulungu.

14. Ndipo Kore mwana wa Imna Mlevi, wa ku cipata ca kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulikitsa.

15. Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Minyamini, ndi Yesuwa; ndi Semaya, Amariya, ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akuru monga ang'ono;

16. pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa ali yense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa nchito yace pa tsiku lace, kukacita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 31