Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 31:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Citatha ici conse tsono, Aisrayeli onse opezekako anaturuka kumka ku midzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efraimunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israyeli anabwerera, yense ku dziko lace ndi ku midzi yao.

2. Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wace, ndi ansembe ndi Alevi, acite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, ku zipata za cigono ca Ambuye.

3. Naikanso gawo la mfumu lotapa pa cuma cace la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova.

4. Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'cilamulo ca Yehova.

5. Ndipo pobuka mau aja, ana a Israyeli anapereka mocuruka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uci, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mocuruka.

6. Ndi ana a Israyeli ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyuru miyuru,

7. Mwezi wacitatu anayamba kuika miyalo ya miyuruyi, naitsiriza mwezi wacisanu ndi ciwiri.

8. Ndipo pamene Hezekiya ndi akuru ace anadza, naona miyuruyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ace Aisrayeli.

9. Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuruyi,

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 31