Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 30:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,

10. Ndipo amtokoma anapitira m'midzi m'midzi mwa dziko la Efraimu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.

11. Komatu ena a Aseri ndi Manase ndi a Zebuloni anadzicepetsa, nadza ku Yerusalemu.

12. Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kucita cowauza mfumu ndi akuru mwa mau a Yehova.

13. Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kucita madyerero a mkate wopanda cotupitsa mwezi waciwiri, msonkhano waukuru ndithu.

14. Ndipo anauka nacotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nacotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kedroni.

15. Pamenepo anaphera Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi waciwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anacita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza ku nyumba ya Yehova.

16. Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa cilamulo ca Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira ku dzanja la Alevi.

17. Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatula; potero Alevi anayang'anira kupha za Paskha kwa ali yense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.

18. Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efraimu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretsa, koma anadya Paskha mosati monga munalembedwa.

19. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wace kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ace, cinkana sanayeretsedwa monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.

20. Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawaciritsa anthu.

21. Ndipo ana a Israyeli opezeka m'Yerusalemu anacita madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe cacikuru; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoyimbira zakuliritsa kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 30