Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 13:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tiri nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi. Alevi, m'nchito mwao,

11. nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za pfungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi coikapo nyali cagolidi ndi nyali zace, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga cilangizo ca Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.

12. Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ace, ndi malipenga oliza nao cokweza, kukulizirani inu cokweza. Ana a Israyeli inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.

13. Koma Yerobiamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.

14. Ndipo poceuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; napfuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.

15. Pamenepo amuna a Yuda anapfuula cokweza; ndipo popfuula amuna a Yuda, kunacitika kuti Mulungu anakantha Yerobiamu ndi Aisrayeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.

16. Ndipo ana a Israyeli anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.

17. Ndipo Abiya ndi anthu ace anawakantha makanthidwe akuru; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazanaasanu a Israyeli.

18. Momwemo anacepetsedwa ana a Israyeli nthawi ija, nalakika ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.

19. Ndipo Abiya analondola Yerobiamu, namlanda midzi yace, Beteli ndi miraga yace, ndi Yesana ndi miraga yace, ndi Efroni ndi miraga yace.

20. Ndi Yerobiamu sanaonanso mphamvu m'masiku a Abiya, namkantha Yehova, wa iye.

21. Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana amuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana akazi khumi mphambu asanu ndi mmodzi.

22. Macitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ace, ndi mau ace, alembedwa m'buku lomasulira la mneneri Ido.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 13