Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 9:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'cuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Gileadi.

2. Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ace, nupite naye ku cipinda cam'katimo.

3. Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pace, nunene, Atero Yehova; Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israyeli. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osacedwa,

4. Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Gileadi.

5. Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndiri ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa Inu, kazembe.

6. Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pace, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli.

7. Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere cilango ca mwazi wa: atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli.

8. Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israyeli.

9. Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Basa mwana wa Ahiya.

10. Ndipo agaru adzamudya Yezebeli pa dera la Yezreeli, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa.

11. Ndipo Yehu anaturukira kwa anyamata a mbuye wace, nanena naye wina, Mtendere kodi? anakudzera cifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ace.

12. Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine cakuti cakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 9