Ndipo Yehu anaturukira kwa anyamata a mbuye wace, nanena naye wina, Mtendere kodi? anakudzera cifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ace.